1.The Opening

  1. M’dzina la Mulungu, Mwini Chifundo ndi Mwini Chisoni Chosatha
  2. Kuyamikidwandikwa Mulungu,Ambuyewachilengedwe
  3. Mwini Chifundo ndi Mwini Chisoni Chosatha
  4. Mfumu ya tsiku la Chiweruzo
  5. Inu nokha tikulambirani ndipo ndi kwa Inu nokha kumene timapempha chithandizo
  6. Tilangizeni njira yanu yoyenera
  7. Njira ya iwo amene mwawakonda osati ya iwo amene adalandira mkwiyo wanu kapena anasokera