101.The Calamity

  1. Tsiku louka kwa akufa
  2. Kodi tsiku louka kwa akufa ndi chiyani
  3. Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze iwe kuti tsiku louka kwa akufa ndi chiani
  4. Ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati dzombe louluka paliponse
  5. Ndi mapiri adzakhala ngati fumbefumbe za ubweya
  6. Ndipo iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzakhala wolemera
  7. Adzakhala ndi moyo wa chimwemwe ndi chisangalalo
  8. Koma iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzapezeka wopepuka
  9. Mudzi wake udzakhala dzenje lamoto
  10. Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze zinthu zonsezi
  11. Ndi moto wa malawi osatha