102.Competition

  1. Mpikisano wosonkhanitsa chuma cha padziko wakutangwanikitsani inu
  2. Mpaka pamene inu mulowa m’manda
  3. Iyayi! Inu mudzadziwa
  4. Kachiwiri, Iyayi! Inu mudzadziwa
  5. Iyayi! Inu mukanadziwa kwenikweni
  6. Ndithudi inu mudzaona moto woyaka
  7. Kachiwiri inu mudzauona ndi maso anu
  8. Ndipo patsiku limeneli inu mudzafunsidwa za chisangalalo chimene munali kuchita