104.The Traducer

  1. Tsoka kwa aliyense amene amajeda ndi kuononga mbiri ya anzake
  2. Amene amasonkhanitsa chuma chake ndi kumachiwerenga
  3. Iye amaganiza kuti chuma chake chidzamuchititsa iye kukhala ndi moyo wamuyaya
  4. Iyayi! Ndithudi iye adzaponyedwa ku moto woononga
  5. Kodi chidzakuuza kuti moto woononga ndi chiyani
  6. Ndi moto wa Mulungu umene Mwini wake anauyatsa
  7. Umene umafuka m’mitima ya anthu
  8. Ndithudi udzawatsekereza mbali iliyonse
  9. M’sanamila zoima