107.Almsgiving

  1. Kodi wamuona munthu amene amakana kuti kuli tsiku la chiweruzo
  2. Iye ndiye amene amazunza mwana wamasiye
  3. Ndipo sakakamiza anthu ena kuti azidyetsa anthu osauka
  4. Motero tsoka kwa iwo amene amapemphera
  5. Amene salabadira mapemphero awo
  6. Amene amachita zabwino pofuna kuti ena awaone
  7. Ndipo amakana kupereka chaulere