4.The Women

  1. oh inu anthu! Muopeni Ambuye wanu amene anakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo kuchokera kwa munthu ameneyu, Iye analenga mkazi wake. Ndipo kudzera mwa iwo, Iye adadzadza dziko lonse lapansi ndi anthu amuna ndi akazi osawerengeka. Opani Mulungu, dzina limene mumadandaulirana wina ndi mnzake. Ndipo lemekezani chibale. Ndithudi Mulungu amakuyang’anirani nthawi zonse
  2. Apatseni ana a masiye chuma chawo akafika msinkhu woyenera. Musasinthitse choipa ndi chabwino ndipo musadye chuma chawo pamodzi ndi chanu chifukwa kutero, ndithudi, ndi tchimo lalikulu
  3. Ngati inu muopa kuti simungathe kuchita chilungamo ndi ana a masiye, kwatirani mkazi amene mungamukonde awiri, atatu kapena anayi. Koma ngati inu muopa kuti simudzatha kuchita chilungamo, kukwaniritsa zonse bwinobwino, kwatirani mmodzi yekha kapena wina wa a kapolo a chitsikana amene muli nawo. Chimenechi chidzakhala chapafupi kwa inu kuti musalephere kutsata njira ya chilungamo
  4. Apatseni akazi mphatso yawo monga mphatso yaulere. Koma ngati iwo, mwa chifuniro chawo, asankha kukugawiraniko gawo la mphatsoyi, idyani mosangalala ndi mwa ubwino
  5. Musawapatse anthu ozerezeka katundu amene Mulungu wakupatsani kuti muziwathandizira, koma inu muyenera kuwasamala ndi kuwaveka kuchokera ku phindu la katunduyu ndipo lankhulani nawo mawu abwino a chifundo
  6. Aikeni ana a masiye pa mayesero mpakana pamene afika poti atha msinkhu. Ngati inu muona kuti ndi a maganizo okhazikika, apatseni chuma chawo ndipo musawaonongere iwo chuma chawo asanathe msinkhu. Munthu amene ali olemera asagwiritse ntchito katundu wa ana a masiye amene ali kumuyang’anira ndipo munthu osauka agwiritse ntchito chuma cha ana a masiye mosamala ndi mwa chilungamo. Pamene inu muwapatsa chuma chawo, itanani ena kuti akhale mboni; Mulungu ndi wokwana kukhala mboni pa zonse zimene muchita
  7. Amuna adzakhala ndi gawo mu katundu amene makolo ndi abale awo asiya ndipo akazi adzakhala ndi gawo mu katunduamenemakolondiabaleawoasiya. Kayakatunduyo ndi wochepa kapena wambiri, onse ayenera kulandira gawo lawo malinga ndi malamulo
  8. Ngati a chibale, a masiye kapena osauka alipo pamene ali kugawa chuma cha masiye, agawireniko nawonso ndipo alankhuleni ndi mawu abwino
  9. Alekeni iwo amene amafunira zabwino ana awo, pamene iwo akufa, kuti asamale posawalakwira ana amasiye. Alekeni kuti aope Mulungu ndi kunena zinthu zokhazikitsa choonadi
  10. Kwa iwo amene amadya chuma cha ana a masiye mopanda chilungamo amameza moto m’mimba mwawo ndipo iwo adzalowa m’malawi a moto wa ku Gahena
  11. Mulungu wakulamulirani motere pankhani za ana anu: Mwana wa mwamuma adzalandira magawo awiri kuposa mwana wa mkazi. Ndipo ngati ana a akazi apitirira awiri, iwo adzalandira magawo awiri pa magawo atatu a katundu wosiyidwa koma ngati alipo mwana mmodzi yekha wamkazi, adzalandila theka ndipo makolo ake awiri, aliyense mwa iwo adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi – muzimene adasiya malemuyo ngati malemuyo ali ndi mwana. Koma ngati alibe mwana ndipo makolo ake ndiwo amene ayenera kulandira katundu wake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo atatu. Ngati iye ali ndi abale ake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi atatha kukwaniritsa lonjezo la malemu ndiponso kubweza ngongole. Inu simudziwa kuti pakati pa makolo anu ndi ana anu amene ali wa phindu ndi inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wanzeru ndi wodziwa chilichonse
  12. Inu mudzalandira theka la chuma chimene akazi anu adasiya, ngati iwo alibe mwana. Ngati ali ndi mwana, inu mudzalandira gawo limodzi la magawo anayi la zimene mkaziyo wasiya pambuyo popereka zimene analonjeza ndi kubwezera ngongole. Nawo akazi anu adzapeza gawo limodzi m’magawo anayi muzimene mwasiya ngati mulibe mwana. Koma ngati muli ndi mwana, iwo, akaziwo, adzapeza gawo limodzi la magawo asanu ndi atatu a zimene mwasiya, pambuyo popereka zimene mudalonjeza ndi kubwezera ngongole. Ngati mwamuna kapena mkazi ndi yemwe wasiya katundu ndipo alibe mwana kapena mdzukulu, koma ali ndi mchimwene wake kapena mchemwali wake, aliyense wa iwo adzapeza gawo limodzi m’magawo asanu ndi limodzi, ndipo ngati adali ambiri koposa apo adzagawana gawo limodzi la magawo atatu pambuyo popereka zimene analonjeza kapena kubwezera ngongole mosabweretsa mavuto. Limeneli ndi lamulo lochokera kwa Mulungu, Mulungu ndi wodziwa ndi woleza mtima
  13. Awa ndi malire a Mulungu. Ndipo aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake adzaikidwa m’minda yoyenda mitsinje pansi pake kumene adzakhalako nthawi zonse. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu
  14. Koma iye amene amanyoza Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amalumpha malire ake, adzamuponya ku moto wa ku Gahena ndipo adzakhala komweko mpaka kalekale ndipo iye adzalandira chilango chochititsa manyazi
  15. Ndipo iwo, mwa akazi anu, amene achita chigololo, pezani mboni zokwanira zinayi zochokera pakati panu ndipo ngati iwo apereka umboni wotsimikiza, asungeni kunyumba zawo mpaka pamene imfa iwapeza kapena mpaka pamene Mulungu alamula kwa iwo njira ina
  16. Ndipo ngati anthu awiri achita chigololo pakati panu, alangeni onse awiri. Ngati iwo alapa ndi kusiya njira zawo zoipa, asiyeni. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha
  17. Mulungu amavomera kulapa kwa amene achita zoipa mosazindikira ngati alapa mwamsanga. Ndi iwo amene Mulungu adzawakhululukira ndipo Mulungu ndi wodziwa ndiponso wanzeru
  18. Kulibe phindu kulapa kwa iwo amene amachita zinthu zoipa mpaka pamene imfa imupeza wina wa iwo ndipo ati: “Tsopano ndalapa,” kapena kwa iwo amene amafa ali osakhulupirira. Kwa iwo Ife tawakonzera chilango chowawa
  19. oh inu anthu okhulupirira! Inu simuloledwa kulowa chokolo chokakamiza ndipo musawazunze ndi cholinga choti muwalande zina zimene mudawapatsa pokhapokha ngati achita chigololo. Ndipo khalani nawo mwa mtendere. Ngati simukuwafuna, mwina mungachide chinthu chimene Mulungu waikamo zabwino zambiri
  20. Koma ngati inu mufuna kusudzula mkazi ndi cholinga chokwatira mkazi wina ndipo mutampatsa mmodzi mwa iwo chuma chochuluka, ngati mphatso ya ukwati, musatenge chilichonse mwa chumacho. Kodi inu mungakhale mopanda chilungamo ndikuwonetsa kuchimwa poyera
  21. Kodi inu mungalande bwanji chuma pamene munali kugonera limodzi, ndipo iwo adakupatsani chipangano chotsimikizika
  22. Ndipo musakwatire mkazi amene adakwatiwapo ndi abambo anu, kupatula zimene zidatha kale. Ndithudi zinali zochititsa manyazi; zonyansa ndiponso njira yauchimo
  23. Inu mwaletsedwa kukwatira awa: Amayi anu, ana anu a akazi, alongo anu, azakhali anu, achemwali amayi anu, ana akazi achimwene anu, ana akazi a alongo anu, amayi amene adakuyamwitsani, akazi amene mudayamwitsidwa nawo bere limodzi, apongozi anu, ndi ana a akazi owapeza amene muli kuwasunga amene anabereka akazi amene mwawakwatira. Koma ngati simunagonepo ndi amai awo palibe choletsa kwa inu kuwakwatira atsikanawo. Kukwatiraakaziaanaanuamunaamenemudaberekainundi akazi awiri amimba imodzi nthawi imodzi ndi koletsedwa kupatula zimene zinachitika kale. Ndithudi Mulungu ndi okhululukira ndi wa chisoni chosatha
  24. Ndipo ndikoletsedwa kukwatira akazi okwatiwa kupatula amene ali m’manja mwanu ngati akapolo. Limeneli ndi lamulo la Mulungu kwa inu. Ndipo ndi kololedwa kwa inu kukwatira wina aliyense amene sanatchulidwe pamwambapa ngati inu muwapatsa mphatso ya ukwati kuchokera ku chuma chanu mu njira yabwino osati ya chiwerewere. Amene muwakwatira , apatseni mphatso yawo ya ukwati motsatira malamulo. Koma pamene mphatso itchulidwa, sizolakwika kwa inu ngati mugwirizana. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa, ndi Waluntha
  25. Ndipo ngati wina wa inu alibe mwayi woti nkukwatira mkazi wokhulupirira amene ndi mfulu, mukhoza kukwatira mwa atsikana anu wokhulupirira kuchokera kugulu la akapolo amene muli nawo, ndipo Mulungu amadziwa zonse za chikhulupiriro chanu ndipo inu ndinu amodzi. Akwatitseni ndi chilolezo cha ambuye awo ndipo muwapatse mphatso yawo ya ukwati mwa chilungamo. Iwo ayenera kudzisunga, osati a chiwerewere kapena wochita chibwenzi. Ndipo ngati akwatiwa ndipo achita chigololo, chilango chawo ndi theka la chilango chimene mfulu ya ikazi ingalandire. Ichi chikhudza iye amene aopa kupwetekeka pakati pa inu. Koma ndi kwabwino ngati inu mudziletsa ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
  26. Mulungu afuna kuti akufotokozereni inu ndi kukutsogolerani ku njira za iwo amene adalipo inu musanadze ndi kukukhululukirani inu. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi wanzeru
  27. Mulungu afuna kukukhululukirani inu koma iwo amene amatsatira zilakolako zawo amafunisitsa mutasiya njira yoyenera
  28. Mulungu afuna kukupeputsirani malamulo ake chifukwa munthu analengedwa wofoka
  29. oh inu anthu okhulupirira! Musadye chuma cha anzanu mopanda chilungamo ngakhale kuti ndi malonda amene mwagwirizana pakati panu. Ndipo musawonongane wina ndi mzake. Ndithudi Mulungu ndi wa chifundo chosatha kwa inu
  30. Ndipo aliyense amene achita izi mwamtopola kapena mwakusowa chilungamo, Ife tidzamulowetsa kumoto ndipo kutero si chinthu chovuta kwa Mulungu
  31. Ngati inu mupewa machimo akuluakulu amene mukuletsedwa, Ife tidzakukhululukirani machimo anu ndipo tidzakulowetsani kukhomo lolemekezeka
  32. Ndipo musasirire zokoma zimene Mulungu wawapatsa ena a inu kuposa anzawo. Kwa amuna kuli gawo kuzimene amachita, nawonso akazi ali ndi gawo muzimene amachita ndipo mupempheni Mulungu kuti akupatseni zabwino zake. Ndithudi Mulungu amadziwa chinthu chilichonse
  33. Ndipo kwa aliyense tamuikira abale olandira chuma chimene chasiyidwa ndi makolo ndi abale. Ndipo iwo amene mwachita nawo chipangano, apatseni gawo lawo nawonso kuti alandire. Ndithudi Mulungu ndi mboni pa zinthu zonse
  34. Anthu amuna ndi atetezi ndi osamala anthu akazi chifukwa Mulungu wawalemekeza ena kuposa anzawo ndiponso chifukwa cha chuma chawo chimene amagwiritsa ntchito. Motero akazi ochita zabwino ndipo amene amamvera, amasunga pamene amuna awo palibe, ndi zimene Mulungu awalamulira kuti azisunge. Ndipo akazi amene mukuona kuti samvera achenjezeni ndipo ngati iwo sasintha asiyeni agone pa okha ndipo ngati sasinthabe amenyeni. Koma ngati iwo akumverani, musawafunire njira yachabe. Ndithudi Mulungu ndi wapamwamba ndi wamkulu
  35. Ndipo ngati inu muopa kuti asiyana, sankhani nkhoswe kuchokera kwa m’bale wa mwamuna ndiponso nkhoswe kuchokera kwa m’bale wa mkazi ngati iwo akufuna kuyanjanitsidwa, ndipo Mulungu adzawayanjanitsa pakati pawo. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa ndi wozindikira
  36. Pembedzani Mulungu ndipo musamuphatikize Iye ndi china chilichonse ndipo chitani zabwino kwa makolo anu ndi achibale, kwa a masiye ndi kwa osauka, ndi kwa anzanu amene muli nawo pafupi kapena kutali ndi anzanu okhala nawo pafupi, ndi kwa a paulendo ndi kwa akapolo anu. Ndithudi Mulungu sakonda anthu a mtudzu ndi odzikundikira
  37. Iwo amene ndi oumira ndipo amauza anzawo kuti akhalenso oumira, amene amabisa chuma chimene Mulungu adawapatsa mwachifundo chake. Ndipo Ife tawakonzera anthu osakhulupirira chilango chochititsa manyazi
  38. Ndi iwo amene amaononga chuma chawo modzionetsera kwa anthu, ndipo sakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chiweruzo; ndipo aliyense amene asankha Satana kukhala bwenzi lake, wasankha bwenzi loopsya
  39. Kodi iwo akadataya chiyani ngati akadakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chiweruzo ndi kupereka muzinthu zimene Mulungu adawapatsa iwo kuti ziziwathandiza? Mulungu amawadziwa onse
  40. Ndithudi! Mulungu sapondereza malipiro ngakhale a kanthu kochepa, ndipo ngati muli zabwino Iye adzakaonjezera malipiro ake ndipo amapereka kuchokera kwa Iye malipiro ochuluka
  41. Kodi zidzakhala bwanji pamene tidzabweretsa mboni kuchokera ku anthu a mtundu uliwonse ndipo tikubweretsa iwe kuti uzakhale mboni yowatsutsa
  42. Patsikulo onse amene sadakhulupilire ndipo sanamvere Mtumwi adzafunitsitsa akadaundiridwa m’nthaka koma iwo sadzabisa china chilichonse kwa Mulungu
  43. oh inu anthu okhulupirira! Musayandikire mapemphero pamene muli oledzera mpaka pamene mudziwa tanthauzo la zimene muli nkunena ndiponso pamene mwakhala malo ndi a kunyumba kwanu ndipo simunasambe kupatula pamene muli pa ulendo. Ndipo ngati muli nkudwala kapena muli pa ulendo kapena mmodzi mwa inu wachokera ku chimbudzi kapena mwagona limodzi ndi akazi anu, ndipo simudapeze madzi, tapani dothi labwino ndipo mupukute nkhope ndi manja anu. Ndithudi Mulungu ndi wa chifundo ndi okhululukira
  44. Kodi iwe siunawaone iwo amene adapatsidwa gawo la Buku ali kusochera ndipo akufuna kuti iwe usochere ku njira yabwino
  45. Mulungu amawadziwa bwino adani anu ndipo Mulungu ndi wokwana kukhala Mtetezi ndipo ndi wokwana kukhala Mthandizi
  46. Pakati pa Ayuda pali ena amene amasinthitsa mawu m’malo mwake ndipo amati: “Ife tamva mau ako koma sitikumvera ndipo imva koma usamve chili chonse” ndipo amati: ‘Chenjera, timvere ife ndipo ife tidzakumvera’ ali kupotoza malirime awo ndi cholinga chotukwana chipembedzo. Koma iwo akadati: “Tamva ndipo tatsatira; tiphunzitse ife”; zikadawakhalira bwino kwambiri, koma Mulungu wawatemberera iwo chifukwa chosakhulupirira kwawo motero iwo sakhulupilira koma pang’ono
  47. oh inu anthu amene mudapatsidwa Buku! Khulupirirani zimene tavumbulutsa zimene zitsimikizira Maua Mulunguamenemulinawo, tisadatembenuzenkhope ndikuzibwezera kumbuyo kwake kapena kuwatemberera monga mmene tidawatemberera anthu ophwanya tsiku la Sabata. Ndipo lamulo la Mulungu limatsatidwa ndipo limakwaniritsidwa
  48. Ndithudi Mulungu sakhululukira kuti milungu izipembedzedwa yowonjezera pa Iye koma Iye amakhululukira aliyense amene wamufuna pa machimo ena. Ndipo aliyense amene amapembedza milungu ina yowonjezera pa Iye, iye, ndithudi, wapeka bodza loopsya
  49. Kodi simunaone amene amadziyeretsa okha? Iyayi! Koma Mulungu amayeretsa aliyense amene Iye wamufuna ndipo iwo sadzaponderezedwa ngakhale ndi pang’ono pomwe
  50. Taona mmene iwo amapekera bodza lokhudza Mulungu ndipo zimenezi zikukwanira kukhala tchimo looneka
  51. Kodi siunaone iwo amene adapatsidwa gawo la Buku la Mulungu? Iwo amakhulupirira mafano ndi milungu yabodza ndipo amawauza osakhulupilira kuti ndi otsogozedwa bwino kuposa anthu okhulupirira
  52. Amenewa ndiwo anthu amene Mulungu wawatemberera ndipo aliyense amene atembereredwa ndi Mulungu iwe siungamupezere womuthandiza
  53. Kodi kapena iwo ali ndi gawo mu Ufumu? Zikadatero, iwo sakadawapatsa anthu ngakhale kanthu kakang’ono
  54. Kodi kapena iwo amachitira kaduka anthu mu zinthu zabwino zimene Mulungu wawapatsa? Ife tidawapatsa ana a Abrahamu Buku ndi luntha ndipo tidawapatsa Ufumu waukulu
  55. Ena mwa iwo adakhulupirira iye koma ena a iwo anayang’ana kumbali ndipo Moto ukukwanira kukhala chilango chawo
  56. Ndithudi iwo amene adakana zizindikiro zathu tidzawaotcha ku moto. Nthawi zonse pamene makungu awo azidzapsya, Ife tidzawapatsa makungu ena kuti iwo alawe chilango. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu nthawi zonse ndi Wanzeru
  57. Koma iwo amene amakhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, Ife tidzawalowetsa m’minda yothiriridwa ndi mitsinje yoyenda pansi pake, ndipo adzakhalako mpaka kalekale. Ndipo kumeneko adzakhala ndi akazi oyera ndipo Ife tidzawalowetsa ku mthunzi wabwino kwambiri
  58. Ndithudi Mulungu ali kukulamulirani kuti mubwezere katundu amene mwasunga kwa eni ake ndipo ngati muweruza pakati pa anthu, weruzani mwachilungamo. Ndithudi chilangizo chimene Mulungu akukulangizani ndi chabwino kwambiri. Ndithudi Mulungu amamva nthawi zonse ndipo amaona zinthu zonse
  59. oh inu anthu okhulupirira! Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake ndiponso iwo amene ali ndi udindo pakati panu. Ndipo ngati mutsutsana pa chinthu china chilichonse, chiperekeni icho kwa Mulungu ndi Mtumwi wake ngati inu mumakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Zimenezi zidzakhala zabwino ndi zolungama pomaliza
  60. Kodi iwe wawaona amene amanena kuti amakhulupirira mu zimene zavumbulitsidwa kwa iwe ndi kwa Atumwi ena amene adalipo iwe usanadze ndipo iwo amafunafuna chiweruzo cha oweruza abodza, pamene iwo adalamulidwa kuti awakane iwo? Koma chofuna cha Satana ndi kuwasokeretsa iwo ku njira yoyenera
  61. Ndipo pamene auzidwa “Bwerani ku zimene Mulungu wavumbulutsa ndiponso kwa Mtumwi,” iwe umaona anthu a chinyengo ali kukukana iwe mwamwano
  62. Kodi bwanji, ngati vuto ligwa pa iwo chifukwa cha ntchito zimene adatsogoza manja awo, amadza kwa iwe, kulumbira m’dzina la Mulungu kuti: “Ife sitifuna china chilichonse koma zabwino ndi chigwirizano!”
  63. Awa ndiwo amene Mulungu amadziwa zimene zili m’mitima mwawo. Motero asiye koma uwachenjeze ndipo uwauze mawu ogwira mtima
  64. IfesitidatumizeMtumwialiyense,komakutiatsatiridwe mwa lamulo la Mulungu. Ngati iwo adadzilakwitsa, akanadza kwa iwe kupempha chikhululukiro cha Mulungu ndipo Mtumwi akadawapemphera chikhululukiro cha Mulungu. Iwo akadamupeza Iye wokhululuka ndi wa chisoni
  65. Koma iyayi, pali Ambuye wako, iwo sadzakhala okhulupirira mpaka pamene akusankha iwe kukhala oweruza pa mikangano ya pakati pawo ndipo satsutsa chiweruzo chako, ndipo achivomeleza kwathunthu
  66. Zikadakhala kuti Ife tidawalamulira kuti: “Mudziphe nokha kapena tulukani m’nyumba zanu,” sakadachita kupatula owerengeka okha. Koma ngati iwo akadachita zimene auzidwa zikadakhala bwino kwa iwo, ndipo zikadaonjezera chikhulupiriro
  67. Ndipo ndithudi Ife tikadawapatsa iwo, kuchokera kwa Ife, dipo lalikulu
  68. Ndithudi Ife tikadawatsogolera ku njira yoyenera
  69. Ndipo aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake, ameneyo ndi amene ali pamodzi ndi anthu amene Mulungu wawadalitsa kuchokera ku gulu la Atumwi, anthu a chilungamo, anthu ofera ku nkhondo m’njira ya Mulungu ndi anthu ochita zabwino. Ati bwanji kukoma kukhala mgulu lotere
  70. Ichi ndi chisomo chochokera kwa Mulungu, ndipo Mulungu ndi wokwanira kukhala wodziwa chili chonse
  71. Oh inu anthu okhulupirira! Khalani okonzeka ndipo yendani m’magulu m’magulu kapena pa gulu limodzi lokha
  72. Alipo wina pakati panu amene adzatsalira m’mbuyo. Amene ngati choipa chioneka kwa inu amanena kuti: “Ndithudi Mulungu wandionetsera ine chifundo chifukwa sindinali nawo.”
  73. Koma ngati mtendere wochokera kwa Mulungu ukupezani, ndithudi iye adzanena ngati kuti padalibe ubwenzi pakati pa iye ndi inu ndipo iwo adzati: “Ndikadakhala nawo limodzi, ndithudi ndikadakhala ndi mwayi waukulu.”
  74. Kotero alekeni iwo amene amagulitsa moyo uno ndi moyo umene uli nkudza kuti amenye nkhondo mu njira ya Mulungu. Aliyense amene amenya nkhondo m’njira ya Mulungu ndipo aphedwa kapena apambana, Ife tidzamupatsa dipo lalikulu
  75. Kodi ndi chifukwa chiyani inu simukumenya nkhondo m’njira ya Mulungu pamene anthu ofoka mwa anthu amuna, akazi ndi ana amati: “Ambuye wathu! Tipulumutseni kuchoka kumzinda uwu wa anthu wochita zoipa ndipo tidzutsireni mtetezi wochokera kwa Inu amene adzatithandiza ife.”
  76. Iwo amene akhulupirira amamenya nkhondo m’njira ya Mulungu koma amene sakhulupilira amamenya mu njira ya Satana. Kotero inu menyanani ndi abwenzi a Satana, ndithudi chikonzero cha Satana ndi chopanda mphamvu
  77. Kodi siunaone anthu amene amauzidwa kuti: “Musamenye nkhondo, pempherani mwandondomeko ndipo perekani msonkho wothandizira anthu osauka,” koma pamene iwo adalamulidwa kuti amenye nkhondo, taona; enaaiwoamaopaanthumongamomweamamuopera Mulungu kapenanso kuposa apa. Iwo amati: “Ambuye wathu! Kodi ndi chifukwa chiyani mwatilamula kuti timenye nkhondo? Kodi simungatipatse nthawi yopumula ngakhale yochepa” Nena: “Chisangalalo cha moyo uno ndi chochepa kwambiri. Moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwambiri kwa iye amene amaopa Mulungu ndipo inu simudzaponderezedwa ndi pang’onong’ono pomwe.”
  78. Pali ponse pomwe mungakhale, imfa idzakupezani, ngakhale inu mutadzitsekera mkati mwa nsanja zolimba. Ndipo ngati zabwino ziwapeza, iwo amati: “Izi zachokera kwa Mulungu” koma ngati choipa chiwagwera, iwo amati: “Ichi ndi chochokera kwa iwe.” Nena: “Zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu.” Kodi ndi chiani chawapeza anthu awa kuti sangathe kuzindikira china chiri chonse
  79. Chilichonse chabwino chimene chidza pa iwe ndi chochokera kwa Mulungu, ndipo choipa chimene chikupeza ndi chochokera kwa iwe mwini. Ndipo Ife takutumiza iwe ngati Mtumwi kwa anthu onse. Ndipo Mulungu akwana kukhala mboni
  80. Aliyense amene amvera Mtumwi ndithudi amvera Mulungu ndipo iye amene safuna kukumvera iwe, Ife sitidakutumize kuti ukhale wowayang’anira ayi
  81. Iwo amati: “Ife ndife omvera” koma iwo akangochoka kwa iwe, ambiri a iwo amachita chiwembu usiku pochita zinthu zimene siukunena. Koma Mulungu amalemba ziwembu zawo zonse zomwe amachita usiku. Kotero aleke okha ndipo ika chikhulupiliro chako mwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi
  82. Kodi iwo salingalira za Korani? Ilo likadakhala kuti silinachokere kwa Mulungu, iwo akadapeza mu ilo kusemphana kwambiri
  83. Pamene iwo amva nkhani iliyonse ya mtendere kapena yochititsa mantha, iwo amaiulutsa koma iwo akanaipereka kwa Mtumwi kapena kwa amene ali ndi udindo pakati pawo kapena anthu amene amafufuza bwino nkhani, akadadziwa. Ndipo pakadapanda chisomo ndi chisoni cha Mulungu pa inu, inu mukanatsatira Satana kupatula anthu ochepa okha
  84. Motero menya nkhondo mu njira ya Mulungu, iwe siudzafunsidwa za munthu wina ayi koma za iwe wekha ndipo alimbikitse okhulupirira kuti mwina Mulungu adzagonjetsa anthu osakhulupirira. Mulungu ndi wamphamvu kwambiri ndi Waukali polanga
  85. Aliyense amene amathandiza kuchita ntchito zabwino adzalandira gawo lake la ntchitoyo, ndipo aliyense amene amathandiza kuchita ntchito zoipa naye adzakhala ndi gawo la uchimo. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu yochita chinthu china chilichonse
  86. Ngati munthu akulonjerani onetsetsani kuti malonje anu ndi abwino kuposa malonje ake kapena mumubwezere monga momwe wakulonjererani. Ndithudi Mulungu amasunga chiwerengero cha zinthu zonse
  87. Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ndithudi Iye adzakusonkhanitsani nonse pamodzi patsiku louka kwa akufa, tsiku lopanda chikaiko. Kodi ndani amalankhula zoona kuposa Mulungu
  88. Kodi mwatani kuti mukhale ogawikana magulu awiri pa nkhani ya anthu a chinyengo? Mulungu, mwini wake wawataya chifukwa cha ntchito zawo zoipa. Kodi inu mufuna kumutsogolera iye amene Mulungu wamusokeretsa? Inu simudzapeza njira ina iliyonse
  89. Iwo afuna kuti iwe usakhulupirire monga momwe iwo sadakhulupirire kuti mulingane. Iwe usapalane nawo ubwenzi ayi mpaka pamene asiya nyumba zawo chifukwa cha njira ya Mulungu. Koma ngati iwo akuthawani, agwireni ndipo muwaphe pali ponse pamene muwapeze ndipo musafune abwenzi kapena okuthandizani pakati pawo
  90. Kupatula okhawo amene gulu lina limene liri pakati panu ndipo inu mwachita nawo pangano lokhazikitsa mtendere kapena adza kwa inu chifukwa mitima yawo yawaletsa kuti amenyane nanu kapena kumenyana ndi anthu a mtundu wawo. Mulungu akadafuna akadawapatsa iwo mphamvu zoti akugonjetseni inu, kotero akadamenyana nanu. Choncho ngati atalikirana nanu ndipo asiya kumenyana nanu ndi kukuonetsani mtendere, Mulungu wakulamulirani kuti musawaononge
  91. Mudzawapeza ena ali kufuna chitetezo chanu ndiponso chitetezo chochokera kwa anthu awo. Nthawi iliyonse akayesedwa iwo amapita mwamsangamsanga. Ngati iwo sachoka kwa inu ndiponso ngati iwo sakhazikitsa mtendere ndi inu kapena kusiya nkhondo ndi inu, agwireni ndi kuwapha pali ponse pamene muwapeza. Pa anthu otere, Ife takupatsani chilolezo chomenyana nawo
  92. Ndi chinthu choletsedwa kuti munthu wokhulupirira aphe mzake wokhulupirira kupatula mwangozi. Ndipo aliyense amene, mwangozi, akupha munthu wokhulupirira ayenera kumasula kapolo wokhulupirira m’modzi ndi kulipira ndalama zopepesera ku banja la ophedwayo, kupatula ngati iwo asankha kuti amukhululukira munthu wakuphayo. Ngati malemuyo anali wochokera kwa adani anu ndipo anali wokhulupirira, chilango chake ndi kumasula kapolo m’modzi wa wokhulupirira. Koma ngati malemuyo anali ochokera ku mtundu wa athu ogwirizana nawo, ndalama za chipepeso ziyenera kuperekedwa kubanja la munthu wakufayo ndi kumasula kapolo mmodzi wa wokhulupirira. Ngati munthu sangathe kupeza izi, ayenera kusala miyezi iwiri motsatizana ndi cholinga chopeza chikhululukiro kwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi Wodziwa ndi Waluntha
  93. Ndipo aliyense amene apha munthu wokhulupirira mwadala, mphotho yake ndi kupsya ku moto wa ku Gahena ndipo adzakhala komweko ndipo mkwiyo ndi temberero la Mulungu zili pa iye ndipo chilango chowawa chili kukonzedwa chifukwa cha iye
  94. oh inu anthu okhulupirira! onetsetsani kuti pamene mupita kukamenya nkhondo m’njira ya Mulungu, kuti musanene kwa iwo amene akhulupirira kuti ndi osakhulupirira pofuna kuti mupeze katundu wosakhalitsa wa mdziko lino. Kwa Mulungu kuli zinthu zambiri zabwino. Monga mmene iye ali, nanunso mudali wosakhulupirira m’masiku adzana koma tsopano Mulungu wakupatsani chisomo chake pokutsogolerani ku njira yoyenera. Kotero musachite tsankho! Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
  95. Anthu okhulupirira amene akhala, safanana kupatula iwo amene ali ndi bvuto ndi amene amenyana nkhondo m’njira ya Mulungu ndi chuma chawo ndi iwo eni. Mulungu adawakweza pamwamba iwo amene amamenya nkhondo ndi chuma chawo pamodzi ndi iwo eni kuposa iwo amene akhala kunyumba. Kwa aliyense, Iye walonjeza malipiro abwino koma Mulungu wawapatsa mphotho yaikulu amene amalimbikira ndipo amamenya nkhondo m’njira ya Mulungu kuposa amene amakhala kunyumba
  96. Adzapeza maudindo kuchokera kwa Iye, chikhululukiro ndi chisoni. Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha
  97. Ndithudi! Iwo amene angelo amachotsa moyo wawo pamene ali ochimwa, adzafunsidwa kuti: “Mudali kuchita chiyani?” Iwo adzanena: “Tinali opanda mphamvu ndi oponderezedwa padziko lapansi.” Angelo adzati kwa iwo: “Kodi dziko la Mulungu silinali lotambasuka kuti inu mukadasamuka?” Iwo mudzi wawo ndi Gahena. Malo oipa kwambiri ofikirako
  98. Kupatula anthu ofoka pakati pa amuna, akazi ndi ana amene alibe mphamvu kapena njira zothawira
  99. Kwa otere pali chikhulupiriro choti Mulungu adzawakhululukira ndipo Mulungu ndi wachisoni ndi wokhululuka nthawi zonse
  100. Iye amene asamuka kwawo mu njira ya Mulungu adzapeza padziko lapansi malo ochuluka othawirako ndi katundu wochuluka. Ndipo iye amene asamuka chifukwa cha Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo imfa impeza, ndithu malipiro ake ali ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wokhululuka ndi wachisoni chosatha
  101. Ndipo pamene inu muyenda padziko lapansi sikulakwa kwa inu kupungula mapemphero ngati muopa kuti anthu osakhulupirira akuvutitsani. Ndithudi anthu osakhulupirira ndi adani anu enieni
  102. Pamene iwe uli pakati pawo ndipo uli kuwatsogolera pa mapemphero, lola gulu lina la iwo kuti liime pamodzi ndi iwe, atanyamula zida zawo za nkhondo. Akatha kugwetsa nkhope zawo pansi apite kumbuyo kwanu ndipo libwere gulu lina limene silinapemphere kuti lipemphere nawe, ayenera kukhala tcheru ndi kutenga zida zawo za nkhondo. Anthu osakhulupirira amafuna inu mutaiwala zida zanu ndi katundu wanu kuti akukantheni nthawi imodzi, koma palibe cholakwa ngati musiya zida zanu chifukwa cha mavuto ena monga mvula kapena matenda koma khala tcheru. Ndithudi Mulungu wawakonzera anthu wosakhulupirira chilango chochititsa manyazi
  103. Pamene mumaliza mapemphero, kumbukirani Mulungu pamene muli choimirira, chokhala pansi kapena chogona. Koma pamene muli pabwino, pempherani nthawi zonse. Ndithudi mapemphero ndi udindo umene udaperekedwa kwa anthu okhulupirira kuti azichita pa nthawi zimene zidakhazikitsidwa
  104. Ndipo musafoke pofunafuna mdani. Ngati inu mumva kuwawa nawonso, ndithudi, akumva kuwawa monga mmene mukuonera kuwawa inu. Koma inu muli ndi chiyembekezo chochokera kwa Mulungu chimene iwo alibe. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi wanzeru
  105. Ndithudi Ife tavumbulutsa Buku kwa iwe mwachoonadi kuti uweruze pakati pa anthu pogwiritsa ntchito chimene Mulungu wakulangiza iwe. Motero iwe usawapemphere anthu oipa
  106. Ndipo pempha chikhululukiro cha Mulungu, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni
  107. Ndipo iwe usawaimire iwo amene amasokeretsa miyoyo yawo. Ndithudi Mulungu sakonda munthu wodzipondereza yekha amene amachita zoipa
  108. Iwo akhoza kudzibisa kwa anthu koma sangathe kudzibisa kwa Mulungu chifukwa Iye ali pamodzi ndi iwo pamene akonza chiwembu nthawi ya usiku ndi mawu amene samukondweretsa. Ndipo Mulungu amadziwa zimene iwo amachita
  109. Lo! Inu ndi amene mudawaimirira mu umoyo wa padzikolapansi.Nangakodindaniameneadzawadandaulire, kwa Mulungu pa tsiku la kuuka kwa akufa kapena ndani amene adzakhala mtetezi wawo
  110. Ndipo iye amene achita choipa kapena achimwira mzimu wake koma pambuyo pake apempha chikhululukiro cha Mulungu, adzamupeza Mulungu ali Wokhululuka ndi Wachisoni
  111. Ndipo aliyense amene achita zoipa akudzilakwira yekha. Ndipo Mulungu ndi Waluntha ndi Wanzeru
  112. Ndipo aliyense amene achita zoipa kapena tchimo koma anamizira munthu wina wopanda chifukwa, ndithudi, iye wadzisenzetsa bodza ndi tchimo limene lili loonekera
  113. Koma pakadapanda Chisomo ndi Chisoni cha Mulungu pa iwe gulu lina la iwo likadafuna kuti likusokeretse koma iwo sangasokeretse wina aliyense koma iwo okha, ndipo iwo sangakupweteke iwe ayi. Mulungu wavumbulutsa kwa iwe Buku la luntha ndi kukuphunzitsa iwe zinthu zimene siunali kuzidziwa. Ndipo ubwino wa Mulungu pa iwe ndi waukulu zedi
  114. Mulibe zabwino zambiri muzokambirana zawo za mseri kupatula mwa iye amene amalangiza za kupereka chaulere, kuonetsa chifundo ndi chiyanjanitso pakati pa anthu, ndipo iye amene amachita izi ndi cholinga chokondweretsa Mulungu, Ife tidzampatsa mphotho yaikulu
  115. Ndipo aliyense amene amatsutsa ndi kutsutsana ndi Mtumwi, langizo lathu litaonetsedwa kwa iye ndipo atsatira njira imene siili ya anthu okhulupirira, Ife tidzamusunga mnjira imene wasankha ndipo tidzamuotcha iye ku Moto, malo onyansa kwambiri
  116. Ndithudi! Mulungu sadzakhululukira munthu wopembedza mafano. Iye adzakhululukira wina aliyense amene wamufuna pa machimo ena onse ndipo aliyense amene amalambira milungu ina osati Mulungu, iye wasochera kwambiri kuchokera ku choonadi
  117. Iwo sapembedza china koma milungu ya ikazi m’malo mwa Iye ndipo iwo sapembedza wina koma Satana wogalukira
  118. Mulungu anamutemberera iye ndipo iye adati: “Ine ndidzalanda gawo lina lokhazikika la akapolo ako.”
  119. “Ndithudi ine ndidzawasocheretsa ndipo, ndithudi, ndidzaukitsa zilakolako zawo zopanda pake ndipo, ndithudi, ndidzawalamula kuboola makutu a ng’ombe ndipo, ndithudi, ndidzawalamula kusintha zinthu zimene zinalengedwa ndi Mulungu.” Ndithudi aliyense amene asankha Satana m’malo mwa Mulungu ngati mtetezi wake, iye ndi wotayika kodziwikiratu
  120. Iye akuwalonjeza ndi kuwakhulupiritsa zinthu zopanda pake ndipo malonjezo a Satana si ena koma chinyengo
  121. Malo a anthu otere ndi Gahena ndipo sadzapeza njira yothawira kumeneko
  122. Koma iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, tidzawalowetsa ku Minda yothiriridwa ndi mitsinje ya madzi yoyenda pansi pake ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale. Lonjezo la Mulungu ndi loona. Kodi ndani amene anganene zoona kuposa Mulungu
  123. Sikudzakhala molingana ndi zilakolako zanu kapena za anthu a m’Buku. Iye amene achita zoipa adzalandira zoipa, ndipo sadzapeza wina kukhala omuteteza kapena kumuthandiza iye pambali pa Mulungu
  124. Ndipo aliyense amene amachita ntchito zabwino, mwamuna kapena mkazi, ndipo ndi wokhulupirira, ameneyo ndiye adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pang’ono
  125. Kodi ndani ali ndi chipembedzo chabwino kuposa munthu amene amadzipereka kwathunthu kwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino ndipo amatsatira chikhulupiriro cha Abrahamu wangwiro? Ndipo Mulungu anamusankha Abrahamu kukhala bwenzi lake la pamtima
  126. Mwini wa chilichonse chimene chili mu mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
  127. Iwo amakufunsa malamulo okhudza akazi. Nena: “Mulungu ali kukuuzani za iwo ndi zomwe zikuwerengedwa m’buku zokhudza ana akazi a masiye amene simukuwapatsa zimene zidalamulidwa kwa iwo komabe inu mufuna kuwakwatira ndi ana opanda mphamvu ndi oponderezedwa ndipo kuti muonetse chilungamo kwa ana a masiye. Ndipo zilizonse zabwino zimene muchita, Mulungu amazidziwa.”
  128. Ndipo ngati mkazi aopa kuzunzidwa kapena kusiyidwa ndi mwamuna wake, sichidzakhala chinthu cholakwa kwa iwo awiriwo ngati onse afuna kugwirizana pakati pawo chifukwa mgwirizano ndi wabwino. Ndipo umunthu umalamulidwa ndi umbombo. Koma ngati inu muchita chinthu chabwino ndi kulewa zoipa, ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mukuchita
  129. Inu simudzatha kuchita chilungamo pakati pa akazi anu ngakhale mutafuna kutero. Motero musakondere mbali imodzi ndikumusiya winayo osadziwa chimene chili kuchitika. Ndipo ngati inu muchita chilungamo ndi kuchita chili chonse chabwino ndi kuopa Mulungu, ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
  130. Koma ngati iwo asiyana, Mulungu adzapereka zochuluka kwa aliyense wa iwo kuchokera ku zinthu zake zambiri. Ndipo Mulungu ndi wopereka mowolowa manja kwa zolengedwa zake ndipo ndi Wanzeru
  131. Ndipo mwini wake wa zonse za m’mlengalenga ndi za pa dziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo, Ife tidawalangiza iwo amene analandira Buku inu musadadze ndiponso ndi inu nomwe kuti muziopa Mulungu. Koma ngati mukana, ndithudi, Mulungu ndiye mwini wa zonse zimene zili m’mlengalenga ndi padziko lapansi. Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi otamandidwa
  132. Ndipo mwini wake wa zonse zimene zili mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wokwanira kukhala Mtetezi wanu
  133. Ngati Iye atafuna, akhoza kukuchotsani inu ndi kubweretsa ena. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu yotero
  134. Aliyense amene afuna dipo la moyo uno ndi Mulungu yekha amene amasunga dipo la m’moyo uno ndi umoyo umene uli nkudza. Ndipo Mulungu amamva zonse ndipo amaona zonse
  135. oh inu anthu okhulupirira! Khalani anthu ochita chilungamo ngati mboni za Mulungu ngakhale kuti umboniwo ndi wosakomera inu kapena makolo anu kapena abale anu, kaya iwo ndi wolemera kapena wosauka. Mulungu ndiye Mtetezi wa iwo onse. Motero musatsatire zilakolako zanu ndi kusiya kuchita chilungamo. Ndipo ngati mukapereka umboni wosayenera kapena kukana kupereka, ndithudi Mulungu ali kudziwa ntchito zanu zimene muchita
  136. oh inu anthu okhulupirira! Khulupirirani mwa Mulungundi Mtumwiwakendi Bukulimenewavumbulutsa kwa Mtumwi wake ndi Buku limene Iye adavumbulutsa kale ndipo aliyense amene sakhulupirira Mulungu, Angelo ake, Mabuku ake, Atumwi ake ndi tsiku lomaliza ndithudi wasokera
  137. Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo kenaka akana ndipo akhulupirira ndipo akananso ndipo aonjezera kusakhulupirira, Mulungu sadzawakhululukira kapena kuwatsogolera kunjira ya choonadi
  138. Achenjezeni anthu achinyengo kuti chilango chowawa chili kuwadikira
  139. Iwo amene amasankha anthu osakhulupirira kukhala atetezi awo m’malo mwa anthu okhulupirira, kodi iwo ali kufuna ulemerero kuchokera kwa iwo? Ndithudi ulemerero, mphamvu ndi kuyamikidwa, Mwini wake ndi Mulungu
  140. Ndipo zavumbulutsidwa kale kwa inu m’Buku kuti pamene inu mukumva chivumbulutso cha Mulungu chili kukanidwa kapena kunyozedwa, inu musakhale pa malo amenewo mpaka pamene ayamba kukamba nkhani zina chifukwa mukakhala nawo, mudzakhala ngati iwo. Ndithudi Mulungu adzasonkhanitsa anthu a chinyengo ndi anthu osakhulupirira ku Gahena
  141. Iwo amene amayembekezera ndi kuyang’ana; ndipo ngati Mulungu akupambanitsani, iwo amati: “Kodi ife sitinali kumbali yanu?” Ndipo ngati anthu osakhulupirira apambana, iwo amati kwa iwo: “Kodi ife sitidali ndi mphamvu zoposa inu ndiponso kodi ife sitidakutetezeni kwa anthu okhulupirira?” Mulungu adzaweruza, pakati panu, pa tsiku lakuuka kwa akufa. Ndipo Mulungu sadzawapatsa anthu osakhulupirira njira yoti apambane anthu okhulupirira
  142. Ndithudi anthu a chinyengo afuna kunyenga Mulungu koma ndi Mulungu amene amawanyenga iwo ndipo pamene iwo amaima pamapemphero, amaimirira mwaulesi kuti anthu awaone ndipo sakumbukira Mulungu ngakhale mwapang’ono
  143. Iwo ali kupita uku ndi uko, ndipo sali m’gulu ili ndipo aliyense amene Mulungu wamusocheretsa simungampezere iye njira
  144. oh inu anthu okhulupirira! Musasankhe anthu osakhulupirira kuti akhale abwenzi anu mmalo mwa anthu okhulupirira. Kodi mukufuna kuika umboni woonekera kwa Mulungu wokutsutsani inu
  145. Ndithudi anthu achinyengo adzaponyedwa ku malo apansipansi a ku Moto. Inu simudzawapezera wowathandiza
  146. Kupatula iwo amene alapa zoipa zawo ndi kuchita ntchito zabwino ndipo ayeretsa chipembedzo chawo. Iwo adzakhala pamodzi ndi anthu okhulupirira. Ndipo Mulungu adzawapatsa anthu okhulupirira mphotho yaikulu
  147. Kodi Mulungu angakulangeni bwanji inu ngati muthokoza ndi kukhulupirira mwa Iye? Ndithudi Mulungu amayamika, ndipo ndi Wodziwa zonse
  148. Mulungu sakondwera ndi kuyankhula mawu oipa pagulu kupatula kuchokera kwa amene waponderezedwa. Ndipo Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa zonse
  149. Kaya inu muonetsera pochita zabwino kapena mubisa, kapena mukhululukira zoipa, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wamphamvu zonse
  150. Ndithudi iwo amene sakhulupirira Mulungu ndi Atumwi ake ndipo afuna kusiyanitsa pakati pa Mulungu ndi Atumwi ake ponena kuti: “Ife timakhulupirira mwa ena ndipo sitikhulupirira ena.” Ndipo amafuna kusankha njira yapakati ndi pakati
  151. Amenewa ndithudi ndi osakhulupirira enieni. Ndipo Ife tawakonzera anthu osakhulupirira chilango chochititsa manyazi
  152. Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Atumwi ake ndipo sasiyanitsa pakati pa aliyense wa iwo, Ife tidzawapatsa mphotho zawo ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha
  153. Anthu otsatira a m’Buku akukufunsa iwe kuti uwatsitsire buku kuchokera kumwamba. Ndithudi iwo adafunsa Mose zazikulu kuposa zimenezi pamene iwo adati: “Tionetse Mulungu poyera.” Koma iwo anakanthidwa ndi mphenzi chifukwa cha uchimo wawo. Ndipo iwo adapembedza mwana wa ng’ombe ngakhale analandira zizindikiro zathu. Komabe Ife tidawakhululukira zimenezo. Ndipo tidampatsa Mose mphamvu zooneka
  154. Pokwaniritsa lonjezo, Ife tidakweza pamwamba pawo phiri, ndipo tidati kwa iwo: “Lowani pa chipata mogwetsa nkhope ndi modzichepetsa.” Ndipo Ife tidawalamula kuti: “Musaswe malamulo a tsiku la Sabata.” Ndipo Ife tidatenga lonjezo lokhazikika kuchokera kwa iwo
  155. Chifukwa chakuphwanya pangano lawo ndi kukana zizindikiro za Mulungu ndi kupha Atumwi popanda chilungamo ndi kulankhula kwawo koti: Mitima yathu ndi yokutidwa. Iyayi, Mulungu wamata mitima yawo chifukwa chakusakhulupirira kwawo. Ndipo iwo sakhulupirira kwenikweni koma pang’ono
  156. Ndi chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndi kulankhula zoipa za Maria, tchimo lalikulu
  157. Ndikulankhula kwawo koti: “Ife tidamupha Messiya, Yesu mwana wamwamuna wa Maria, Mthenga wa Mulungu,” koma iwo sadamuphe ayi ndipo sadampachike koma maonekedwe a Yesu anaikidwa pa munthu wina ndipo iwo amene amatsutsa za izo ndi okaika. Iwo sadziwa chili chonse, koma akutsatira nkhani za m’maluwa. Ndithudi iwo sadamuphe ayi
  158. Koma Mulungu adamukweza kudza kwa Iye. Ndipo Mulungu ndi wa mphamvu ndi Wanzeru
  159. Ndipo palibe mmodzi wa anthu a m’Buku amene angakhulupirire mwa iye, asadafe. Ndipo patsiku louka kwa akufa, iye adzakhala mboni yowatsutsa iwo
  160. Chifukwa chakulakwa kwa Ayuda, Ife tidawaletsa chakudya china chabwino chimene chidali chololedwa kwa iwo ndi chifukwa chotsekereza anthu ambiri mnjira ya Mulungu
  161. Ndi kulandira kwawo kwa katapira pamene iwo ataletsedwa kutero, ndi kudya kwawo kwa chuma cha anthu mwachinyengo. Ndipo Ife takonza chilango chowawa cha anthu osakhulupirira amene ali pakati pawo
  162. Koma iwo ozindikira kwambiri amene ali pakati pawo ndi okhulupirira amene amakhulupirira mu zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zimene zidavumbulitsidwa iwe usanadze, ndipo amapemphera nthawi zonse ndikupereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza, awa ndiwo amene Ife tidzawapatsa mphotho yaikulu
  163. Ife tavumbulutsa kwa iwe monga momwe tidavumbulutsira kwa Nowa ndi kwa Atumwi ena amene anadza pambuyo pa iye. Ndipo tidavumbulutsa kwa Abrahamu, Ishimayeli, Isake, Yakobo ndi a mitundu, Yesu, Yobu, Yona, Aroni ndi Solomoni ndipo Davide tidamupatsa Buku la Masalimo
  164. Ndi Atumwi amene Ife takuuza kale mbiri yawo ndi Atumwi amene sitidakuuze ayi, ndipo ndi Mose Mulungu adalankhula naye mwachindunji
  165. Atumwi ngati obweretsa nkhani zabwino kwa mitundu ya anthu ndipo chenjezo kuti iwo asadzakhale ndi chodandaula kwa Mulungu pambuyo pa Atumwi. Ndipo Mulungu ndi Wamphamvu nd Wanzeru
  166. Koma Mulungu achitira umboni pa zimene wavumbulutsakwaiwe, Iyewalitumizandinzeruzakendipo angelo achitira umboni. Ndipo Mulungu ndi wokwana kukhalamboni
  167. Ndithudiiwoamenesakhulupirirandipo amaletsa ena kutsatira njira ya Mulungu, ndithudi, asochera kwenikweni
  168. Ndithudi iwo amene sakhulupirira ndipo adachita zosalungama, Mulungu sazawakhululukira ndipo sadzawatsogolera kunjira ina
  169. Kupatula njira ya ku Gahena, kuti adzakhaleko mpaka kalekale. Ndipo imeneyi ndi ntchito yopepuka kwa Mulungu
  170. oh inu anthu! Ndithudi wadza kwa inu Mtumwi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wanu, motero khulupirirani mwa iye ndipo zonse zidzakhala bwino kwa inu. Ngati inu simukhulupirira ndithudi mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wodziwa chilichonse ndi Wanzeru
  171. oh inu anthu a m’Buku! Musadutse malire a chipembedzo chanu kapena kunena zokhudza Mulungu kupatula choonadi. Messiya Yesu, mwana wa Maria, sadali wina aliyense koma Mtumwi wa Mulungu ndi Mawu ake amene adanena kwa Maria, ndi Mzimu wolengedwa ndi Iye. Kotero khulupirirani mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Ndipo musanene kuti: “Atatu.” Siyani! Zidzakhala bwino kwa inu. Chifukwa Mulungu ndi mmodzi yekha. Ulemerero ukhale kwa Iye. Iye sangakhale ndi mwana. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi wodalirika
  172. Messiya sangakane kukhala kapolo wa Mulungu ndiponso angelo amene ali kufupi ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene amakana kumutumikira Mulungu chifukwa cha kudzikweza, Iye adzawasonkhanitsa onse kudza pamaso pake
  173. Motero iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzawapatsa mphotho zawo mokwanira ndipo adzawalemeretsa iwo mwachisomo chake chochuluka. Koma iwo amene akana kupembedza kapena oyerekedwa, Iye adzawalanga ndi chilango chowawa. Ndipo iwo sadzapeza wina woposa Mulungu kuti awateteze kapena kuwathandiza
  174. oh inu anthu! Ndithudi wadza kwa inu umboni wooneka kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo Ife takutumizirani Muuni woonekera
  175. Motero iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amadzipereka kwathunthu kwa Iye, adzawalowetsa ku chifundo ndi chisomo chake ndi kuwatsogolera kunjira yoyenera
  176. Iwo amakufunsa za malamulo; Nena: “Mulungu akukuuzani za munthu amene alibe makolo kapena mwana. Ngati munthu wa mwamuna akufa, ndipo alibe mwana koma ali ndi mlongo wake, mlongo wake adzalandire theka la katundu amene asiya. Ndipo ngati mkazi sasiya mwana, mlongo wake adzatenga chuma chake. Koma ngati akhala ndi alongo ake awiri, iwo adzalandire magawo awiri a magawo atatu a katundu amene asiya. Ndipo ngati pali abale amuna ndi akazi, mwamuna adzalandira magawo amene angalandire akazi awiri. Mulungu akukulongosolerani kuti musasochere. Ndipo Mulungu ndi wodziwa chilichonse.”